Channel Avatar

HOT 265 @UCg92V8yIZfA_oYuSAYu6MRg@youtube.com

78K subscribers - no pronouns :c

WELCOME TO HOT 265 YOUTUBE CHANNEL. We cover a variety of t


Welcoem to posts!!

in the future - u will be able to do some more stuff here,,,!! like pat catgirl- i mean um yeah... for now u can only see others's posts :c

HOT 265
Posted 1 month ago

Nkhani yangotipeza pompano
A MUMBA APIKISANA NAWO

A Vitumbiko Mumba omwe akufuna kuyimira nawo pa udindo wa wachiwiri kwa mtsogoleri ku chipani cha MCP awayika pa mndandanda wa opikisana.

Polemba pa tsamba lawo la mchezo la Facebook, a Mumba ati awayika pa pepala lovotera usiku wa lachitatu.

223 - 21

HOT 265
Posted 1 month ago

Yemwe akufuna kukapikisana nawo pa chisankho chomwe chipani cha MCP chikhale chikuchititsa pa 8 August, Engineer Vitumbiko Mumba walembera akulu akulu achipanichi kuti aike dzina lake pa mndandanda wa anthu omwe akupikisana nawo pa chisankhochi pofika 12:30 masanawa apo ai akamang'ara kubwalo la milandu.

Malingana ndi kalata yomwe loya yemwe akuimira a Mumba, a Khumbo Soko, walembera chipanichi palibe chifukwa chokwanira chowachotsera a Mumba pa mndandanda wa anthu opikisana nawo pa chisankhochi ndipo akufuna dzina lawo aliike pa mndandandawu.

A Soko ati chipanichi sichinawafotokozere a Mumba zifukwa zomwe awachotsera pa mndandandau ndipo akatengera ndi zomwe bwalo la milandu lagamula dzulo a Mumba akuyenera kupikisana nawo pa chisankhochi.

Koma ena mwa akuluakulu achipanichi awuza Zodiak Online kuti kalatayi sanalandire.

Bwalo la milandu dzulo linagamula kuti Komiti ya chipanichi ilibe mphamvu yoika malamulo oletsa anthu ena kukapikisana nawo pa chisankho chosankha atsogoleri a chipanichi.

87 - 16

HOT 265
Posted 1 month ago

Engineer Vitumbiko Mumba yemwe adawonetsa chidwi chofuna kudzapikisana nawo pa udindo wa wachiwiri kwa mtsogoleri wa chipani cha Malawi Congress Party (MCP) pamsonkhano womwe ukubwera wa zisankho, wachotsedwa pamndandanda wa omwe akupikisana nawo.

Polengeza mayina a anthu oyenerera kupikisana nawo, wapampando wa komiti ya msonkhanowu, Kezzie Msukwa adati mayina omwe atsimikiziridwa kuti adzapikisana nawo pa udindo wa wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko ndi Moses Kunkuyu, Catherine Gotani Hara, Kezzie Msukwa, ndi Kenneth Zikhale Ng’oma. .

Vitumbiko Mumba wakhala akupanga kampeni pa udindo wa wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino ndipo posachedwapa anali ndi msonkhano waukulu mumzinda wa Mzuzu ndipo anali ndi chikhulupiriro kuti apikisana nawo ndi kupambana pa zisankho.

#Hot265

70 - 14

HOT 265
Posted 4 months ago

Breaking news

Mabungwe omwe si aboma okwana 16 ati akufuna mkulu ozenga milandu a Masauko Chamkakala atule pansi udindo wawo chifukwa Amalawi ataya chikhulupiliro mwa iwo.

Malinga ndi mabungwewa, a Chamkakala sakugwiritsa ntchito bwino mphamvu zawo.

Mwachitsanzo, mabungwewa ati a Chamkakala athetsa milandu yambiri ya katangale monga mlandu wa Paramount Holdings Limited, wa a Bakili Muluzi, wa wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino a Saulos Chilima ndi ina opanda zifukwa zokwanira.

Mabungwewa ati pakufunikanso paikidwe ofesi yapadera yoti idziunikira ziganizo zomwe ofesi ya mkulu wozenga milanduyi imapanga.

Polankhulapo, m’modzi mwa akuluakulu a mabungwewa a Willy Kambwandira ati akufunanso ACB ifotokozere Amalawi ndalama zomwe zaonongedwa pa milandu yomwe yathetsedwayi.

Ena mwa mabungwewa ndi ,monga: Youth and Society (YAS), Centre for Social Accountability and Transparency (CSAT), Catholic Commission for Justice and Peace (CCJP), Malawi Economic Justice Network (MEJN), Malawi Health Equity Network(MHEN) ndi National Alliance Against Corruption (NAAC).

68 - 5

HOT 265
Posted 4 months ago

BOMA LIKUFUNA KUCHOTSA MILANDU YA ACHILIMA
https://youtu.be/hJ4Z-MAOrAI?si=DMFh7...

71 - 8

HOT 265
Posted 4 months ago

Breaking
A Malawi 45 omwe akugwira ntchito mdziko la Israel awamanga, kamba kothawa kumalo komwe anapita kukagwira ntchito ndikupita kutawuni kukagwira ntchito malo ena opanda chilolezo.

Mtsogoleri wa a Malawi okhala ku Israel a Austin Chipeta watsimikiza za kumangidwa kwa a Malawi-wa omwe amangidwa ndi nthambi yowona zolowa ndi zotuluka mdzikolo dzulo.

A Chipeta ati a Malawiwa anathawa ku minda kupita kukampani ina yopanga ma bisiketi.

Anthuwa akuyembekezeleka kuwatengela ku khothi.

54 - 24

HOT 265
Posted 5 months ago

A BON KALINDO WAMANGIDWANSO CHIFUKWA CHOPEZEKA NDI MFUTI.

Atafunsidwa kuti apolisi anadziwa bwanji kuti Kalindo ali ndi mfuti.

Kasambara anayankha kuti: " Kalindo anabwera nayo okha mfutiyo pomwe amafuna kuti apasidwe chilolezo".

Khwima Mchizi yemwe akuyimilira Kalindo anafunsa Kasambara kuti pa nthawi imeneyo anawamanga a Kalindo atabwelesa mfuti yo?

Kasambara anauza bwaloli kuti sanamange Kalindo chifukwa anamupatsa mwayi kuti akabweletse zikalata za mfuti wo.

Bwalo loweruza milandu lawuza Kalindo kuti akumuganizira kuti anapezeka ndi mfuti mopanda chilolezo, mu chaka cha 2021.

Boma lidabweletsa m'bwaloli Innocent Kasambara, yemwe ndi wapolisi wakafukufuku.

Kasambara wauza bwaloli kuti akufuna Kalindo akhale mu chitokosi cha apolisi kamba koti mpaka pano , iwo sanawauzebe apolisi komwe anagula kapena kutenga mfutiwo.

Iye anaonjezera kuti apolisi akufuna Kalindo awalondolere komwe anagula mfutiwo.

Atafunsidwa kuti nchifukwa chani akubweletsa nkhaniyi pano, Kasambara ati kuyambira chaka cha 2021, a Kalindo akhala asakuonetsa chidwi chobweletsa mfutiwo.

116 - 26